wachikondi cover art

wachikondi

K
Kamiza Biton

Erstellt am Jun 9, 2026

Songtexte

(intro)
Ayeee yee sisi,sisi, sisiliyaaa.

(Vers1)
Zikomo makolo anga.
Pondilela kufikana Lelo.
Pano ndakula ndine mtsikana Wankulu pano.
zikomo koma simukuyenela kundipangila chisankho.
Simukuyenela kundisankhila mamuna.
Ndine Wankulu ndilindi ufulu ozisankhila mamuna.

(Corus)
Wanga ndimusankha ndekha, ndekha.
ine wanga ndimusankha ndekha, ndekha.
Ndine mtsikana Wankulu wachikondi.
Ndizipezela ndekha, ndekha.
ine ndizipezela ndekha,ndekha.

(Vers2)
Mumadziwa sayizi yachovala changa.
Mumadziwa zomwe ndimakhumba.Koma simungaziwe mamuna ali kumtima kwanga.
Ndiloleni ndizisankhile wachikondi wammoyo mwanga.
Chisankho sapangilana.Ali muntima ndiyekhayo ndikumufuna.
Mulungu wanditsogolela kwa iye.
Olo patavuta,olo zitavuta ndili kakaka.
Ndili nganganga.
Zilibe ntchito Kaya ndimphawi.
Palibe vuto Kaya ndiwotani,Kaya amapanga chani.
Koma ngati mulungu wandilozela kwa iye.
Ndiwoyenela kwaine.
Chomwe tikudziwa mulungu sanganditsogolele.
mnjila yolakwika.

(Corus)
Wanga ndimusankha ndekha, ndekha.
ine wanga ndimusankha ndekha, ndekha.
Ndine mtsikana Wankulu wachikondi.
Ndizipezela ndekha, ndekha.
ine ndizipezela ndekha,ndekha.
Wanga ndimusankha ndekha, ndekha.
ine wanga ndimusankha ndekha, ndekha.
Ndine mtsikana Wankulu
wachikondi Ndizipezela ndekha, ndekha.
ine ndizipezela ndekha,ndekha.
ALEX BITON ON THE BEATS